Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:12-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Aigupto, anatuma makolo athu ulendo woyamba,

13. Ndipo pa ulendo waciwiri Y osefe anazindikirika ndi abale ace; ndipo pfuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.

14. Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wace, ndi a banja lace lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.

15. Ndipo Yakobo anatsikira ku Aigupto; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;

16. ndipo anawanyamula kupita nao ku Sukemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wace wa ndalama kwa ana a Emori m'Sukemu.

17. Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nacuruka m'Aigupto,

18. kufikira inauka mfumu yina pa Aigupto, imene siinamdziwa Yosefe.

19. Imeneyo inacenjerera pfuko lathu, niwacitira coipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.

20. Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wace:

21. ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wace.

22. Ndipo Moseanaphunzira nzeru zonse za Aaigupto; nali wamphamvu m'mau ace ndi m'nchito zace.

23. Koma pamene zaka zace zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwace kuzonda abale ace ana a Israyeli,

24. Ndipo pakuona wina woti alikumcitira cotpa, iye anamcinjiriza, nambwezera cilango wozunzayo, nakantha M-aigupto.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7