Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:10-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.

11. Koma inadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi cisautso cacikuru; ndipo sanapeza cakudya makolo athu.

12. Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Aigupto, anatuma makolo athu ulendo woyamba,

13. Ndipo pa ulendo waciwiri Y osefe anazindikirika ndi abale ace; ndipo pfuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.

14. Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wace, ndi a banja lace lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.

15. Ndipo Yakobo anatsikira ku Aigupto; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;

16. ndipo anawanyamula kupita nao ku Sukemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wace wa ndalama kwa ana a Emori m'Sukemu.

17. Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nacuruka m'Aigupto,

18. kufikira inauka mfumu yina pa Aigupto, imene siinamdziwa Yosefe.

19. Imeneyo inacenjerera pfuko lathu, niwacitira coipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.

20. Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wace:

21. ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wace.

22. Ndipo Moseanaphunzira nzeru zonse za Aaigupto; nali wamphamvu m'mau ace ndi m'nchito zace.

23. Koma pamene zaka zace zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwace kuzonda abale ace ana a Israyeli,

24. Ndipo pakuona wina woti alikumcitira cotpa, iye anamcinjiriza, nambwezera cilango wozunzayo, nakantha M-aigupto.

25. Ndipo anayesa kuti abale ace akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa cipulumutso mwa dzanja lace; koma sanazindikira.

26. Ndipo m'mawa mwace anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; mucitirana coipa bwanji?

27. koma iye wakumcitira mnzace coipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira?

28. 1 Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha M-aigupto dzulo?

29. 2 Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midyani; kumeneko anabala ana amuna awiri.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7