Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 5:31-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lace lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israyeli kulapa, ndi cikhululukiro ca macimo.

32. Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera iye.

33. Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.

34. Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akuru, ndiye Mfarisi, dzina lace Gamaliyeli, mphunzitsi wa cilamulo, wocitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.

35. Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israyeli, kadzicenjerani nokha za anthu awa, cimene muti muwacitire.

36. Pakuti asanafike masiku ana anauka Teuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, ciwerengero cao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pacabe.

37. Atapita ameneyo, anauka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.

38. Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena nchito iyi icokera kwa anthu, idzapasuka;

39. koma ngati icokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.

40. Ndipo anabvomerezana ndi iye; ndipo m'meheadaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kuchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

41. Pamenepo ndipo anapita kucokera ku bwalo la akuru, 1 nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa cifukwa ca dzinalo.

42. Ndipo masiku onse, m'Kacisi ndi m'nyumba, 2 sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 5