Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 5:23-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. nanena, Nyumba yandende tinapeza citsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.

24. Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kacisi ndi ansembe akulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ici cidzatani.

25. Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kacisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.

26. Pamenepo anacoka mdindo pamodzi ndi anyamata; nadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.

27. Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pa bwalo la akuru. Ndipo anawafunsa mkuru wa ansembe,

28. nanena, Tidakulamulirani cilamulire, musaphunzitsa kuchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi ciphunzitso canu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

29. Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.

30. Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpacika pamtengo.

31. Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lace lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israyeli kulapa, ndi cikhululukiro ca macimo.

32. Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera iye.

33. Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.

34. Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akuru, ndiye Mfarisi, dzina lace Gamaliyeli, mphunzitsi wa cilamulo, wocitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.

35. Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israyeli, kadzicenjerani nokha za anthu awa, cimene muti muwacitire.

36. Pakuti asanafike masiku ana anauka Teuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, ciwerengero cao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pacabe.

37. Atapita ameneyo, anauka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 5