18. nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.
19. Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawaturutsa, nati,
20. Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m'Kacisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.
21. Ndipo atamva ici, analowa m'Kacisi mbanda kuca, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene analinaye, nasonkhanitsa a bwalo la akuru, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo.
22. Koma anyamata amene adafikako sanawapeza m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza,