Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 5:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ocokera ku midzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi obvutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anaciritsidwa onsewa.

17. Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a cipatuko ca Asaduki, nadukidwa,

18. nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.

19. Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawaturutsa, nati,

20. Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m'Kacisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.

21. Ndipo atamva ici, analowa m'Kacisi mbanda kuca, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene analinaye, nasonkhanitsa a bwalo la akuru, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo.

22. Koma anyamata amene adafikako sanawapeza m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza,

23. nanena, Nyumba yandende tinapeza citsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.

24. Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kacisi ndi ansembe akulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ici cidzatani.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 5