Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 5:12-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo mwa manja aatumwi zizindikilo ndi zozizwa zambiri zinacitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khumbi la Solomo.

13. Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;

14. ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;

15. kotero kuti ananyamulanso naturuka nao odwala Ifumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale cithunzi cace cigwere wina wa iwo.

16. Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ocokera ku midzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi obvutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anaciritsidwa onsewa.

17. Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a cipatuko ca Asaduki, nadukidwa,

18. nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.

19. Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawaturutsa, nati,

20. Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m'Kacisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.

21. Ndipo atamva ici, analowa m'Kacisi mbanda kuca, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene analinaye, nasonkhanitsa a bwalo la akuru, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo.

22. Koma anyamata amene adafikako sanawapeza m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza,

23. nanena, Nyumba yandende tinapeza citsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.

24. Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kacisi ndi ansembe akulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ici cidzatani.

25. Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kacisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.

26. Pamenepo anacoka mdindo pamodzi ndi anyamata; nadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.

27. Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pa bwalo la akuru. Ndipo anawafunsa mkuru wa ansembe,

28. nanena, Tidakulamulirani cilamulire, musaphunzitsa kuchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi ciphunzitso canu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

29. Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 5