Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 5:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma munthu wina dzina lace Hananiya pamodzi ndi Safira mkazi wace,

2. anagulitsa cao, napatula pa mtengo wace, mkazi yemwe anadziwa, natenga cotsala, naciika pa mapazi a atumwi.

3. Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?

4. Pamene unali nao, sunali wako kodi? ndipo pamene unaugulitsa sunali m'manja mwako kodi? bwanji cinalowa ici mumtima mwako? sunanyenga anthu, komatu Mulungu.

5. Koma Hananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akuru anagwera onse akumvawo.

6. Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, naturuka naye, namuika.

7. Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wace, wosadziwa cidacitikaco, analowa.

8. Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti.

9. Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kuturuka nawe.

10. Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ace, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kuturuka naye, namuika kwa mwamuna wace.

11. Ndipo anadza mantha akuru pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumvaizi.

12. Ndipo mwa manja aatumwi zizindikilo ndi zozizwa zambiri zinacitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khumbi la Solomo.

13. Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 5