Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 3:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo iye anabvomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu.

6. Koma Petro anati, Siliva ndi golidi ndiribe; koma cimene ndiri naco, ici ndikupatsa, M'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda,

7. Ndipo anamgwira Iye ku dzanja lace lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ace ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.

8. Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kacisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.

9. Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 3