Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 3:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zocokera ku nkhope ya Ambuye;

20. ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Kristu Yesu;

21. amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulunguanalankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ace oyera ciyambire.

22. Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu ziri zonse akalankhule nanu.

23. Ndipo kudzali, kuti wamoyo ali yensesamvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.

24. Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuelindi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.

25. Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.

26. Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wace, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zace.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 3