13. Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wace Yesu; amene, inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.
14. Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,
15. ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ici ife tiri mboni.
16. Ndipo pa cikhulupiriro ca m'dzina lace dzina lacelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo cikhulupiriro ciri mwa iye cinampatsa kucira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.