Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 3:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka kuKacisi pa ora lakupembedza, ndilo lacisanu ndi cinai.

2. Ndipo munthu wina wopunduka miyendo cibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kacisi lochedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kacisi;

3. ameneyo, pakuona Petro ndi Yohane akuti alowe m'Kacisi, anapempha alandire caulere.

4. Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife.

5. Ndipo iye anabvomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu.

6. Koma Petro anati, Siliva ndi golidi ndiribe; koma cimene ndiri naco, ici ndikupatsa, M'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda,

7. Ndipo anamgwira Iye ku dzanja lace lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ace ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.

8. Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kacisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 3