Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 28:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. ndi kuti,Pita kwa anthu awa, nuti,Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;Ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;

27. Pakuti mtima wa anthu awa watupatu,Ndipo m'makutu mwao mmolemakumva,Ndipo masoao anawatseka;Kuti angaone ndi maso,Nangamve ndi makutu,Nangazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo Ine ndingawaciritse.

28. Potero, dziwani inu, kuti cipulumutso ici ca Mulungu citumidwa kwa amitundu; iwonsoadzamva. [

29. ]

30. Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yace yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye,

31. ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 28