Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 27:28-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu.

29. Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuce.

30. Ndipo m'mene amarinyero anafunakuthawa m'ngalawa, natsitsira bwato m'nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikuru,

31. Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikari, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.

32. Pamenepo asilikari anadula zingwe za bwato, naligwetsa.

33. Ndipo popeza kulinkuca, Paulo anawacenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi cinai limene munalindira, ndi kusala cakudya, osalawa kanthu.

34. Momwemo ndikucenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa cipulumutsocanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pa mutu wa mmodzi wa inu.

35. Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya.

36. Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga cakudya iwo omwe.

37. Ndipo life tonse tiri m'ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi.

38. Ndipo m'mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m'nyarija.

39. Ndipo kutaca sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mcenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 27