13. Ndipo poomba pang'ono mwela, poyesa kuti anaona cofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.
14. Koma patapita pang'ono idaombetsa kucokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo;
15. ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa.
16. Ndipo popita kutseri kwa cisumbu cacing'ono dzina lace Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma mobvutika;
17. ndipo m'mene adaukweza, anacita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Surti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.
18. Ndipo pobvutika kwakukuru ndi namondweyo, m'mawa mwace anayamba kutaya akatundu;
19. ndipo tsiku lacitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.