Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 27:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.

12. Ndipo popezadooko silinakoma kugonapo nyengo yacisanu, unyinji unacita uphungu ndi kutiamasule nacokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Foinika, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwela.

13. Ndipo poomba pang'ono mwela, poyesa kuti anaona cofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.

14. Koma patapita pang'ono idaombetsa kucokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo;

15. ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa.

16. Ndipo popita kutseri kwa cisumbu cacing'ono dzina lace Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma mobvutika;

17. ndipo m'mene adaukweza, anacita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Surti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.

18. Ndipo pobvutika kwakukuru ndi namondweyo, m'mawa mwace anayamba kutaya akatundu;

19. ndipo tsiku lacitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 27