Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 27:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lace Yuliyo, wa gulu la Augusto.

2. Ndipo m'mene tidalowam'ngalawa ya ku Adramutiyo ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, dnakankha, ndipo Aristarko Mmakedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.

3. Ndipo m'mawa mwace tinangokoceza ku Sidoni; ndipo Yuliyo anacitira Paulo mwacikondi, namlola apite kwa abwenzi ace amcereze.

4. Ndipo pokankhanso pamenepo, tinapita kutseri kwa Kupro, popeza mphepo inaomba mokomana nafe.

5. Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwace kwa Kilikiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mura wa Lukiya.

6. Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Alesandriya, irikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo.

7. Ndipo m'mene tidapita pang'ono pang'ono masiku ambiri, ndi kufika mobvutika pandunji pa Knido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinai pita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;

8. ndipo popaza-pazapo mobvutika, tinafika ku malo ena dzina lace Pokoceza Pokoma; pafupi pamenepo panali mudzi wa Laseya.

9. Ndipo Itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsya ulendowo, popezanso nyengo ya kusala cakudya idapita kale, Paulo anawacenjeza,

10. nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu.

11. Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 27