Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 26:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;

20. komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kucita nchito zoyenera kutembenuka mtima.

21. Cifukwa ca izi Ayuda anandigwira m'Kacisi, nayesa kundipha.

22. Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwacitira umboni ang'ono ndi akuru, posanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananenazidzafika;

23. kuti Kristu akamve zowawa, kuti iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.

24. Koma pakudzikanira momwemo, Festo anati ndi mau akuru, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakucititsa misala.

25. Koma Paulo anati, Ndiribe misala, Festo womvekatu; koma nditurutsa mau a coonadi ndi odziletsa.

26. Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ici Sicinacitika m'tseri.

27. Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? ndidziwa kuti muwakhulupirira.

28. Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang'ono ufuna kundiyesera Mkristu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 26