Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 25:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma ndinawayankha, kuti macitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa comneneraco.

17. Potero, pamene adasonkhana pano, sindinacedwa, koma m'mawa mwace ndinakhala pa mpando waciweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.

18. Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamchulira konse cifukwa ca zoipa zonga ndinazilingirira ine;

19. koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a cipembedzero ca iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.

20. Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi.

21. Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akaturukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara.

22. Ndipo Agripa anati kwa Festo, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 25