Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 25:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma Paulo anati, ndirikuimirira pa mpando waciweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawacitira-kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.

11. Pamenepo ngati ndiri wocita zoipa, ngati ndacita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zacabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditurukira kwa Kaisara.

12. Pamenepo Festo, atakamba ndi aphungu ace, anayankha, Wanena, Ndirurukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.

13. Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bemike anafika ku Kaisareya, nalankhula Festo.

14. Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festo anafotokozera mfumuyo mlandu wace wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felike,

15. amene ansembe akulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wace.

16. Koma ndinawayankha, kuti macitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa comneneraco.

17. Potero, pamene adasonkhana pano, sindinacedwa, koma m'mawa mwace ndinakhala pa mpando waciweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 25