3. tizilandira ndi ciyamiko conse, monsemo ndi ponsepo, Felike womveka inu.
4. Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupempha, ni mutimvere mwacidule ndi cifatso canu.
5. Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;