Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 24:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha cikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;

12. ndipo sanandipeza m'Kacisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda.

13. Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.

14. Koma ici ndibvomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupira zonse ziri monga mwa cilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;

15. ndi kukhala naco ciyembekezo ca kwa Mulungu cimene iwo okhanso acilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.

16. M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale naco nthawi zonse cikumbu mtima cosanditsutsa ca kwa Mulungu ndi kwa anthu.

17. Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zacifundo, ndi zopereka;

18. popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kacisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma panali Ayuda ena a ku Asiya,

19. ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

20. Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza cosalungama cotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akuru,

21. koma mau awa amodzi okha, amene ndinapfuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 24