Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 23:22-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Pamenepo ndipo kapitao wamkuru anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi.

23. Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikari mazana awiri, apite kufikira Kaisareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, acoke ora lacitatu la usiku;

24. ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felike kazembeyo.

25. Ndipo analembera kalata wakuti:

26. Klaudiyo Lusiya kwa kazembe womveketsa Felike, ndikulankhulani.

27. Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikari, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.

28. Ndipo pofuna kuzindikira cifukwa cakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye ku bwalo la akuru ao.

29. Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a cilamulo cao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.

30. Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali ciwembu ca pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 23