Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 22:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Monganso mkulu wa ansembe andicitira umboni, ndi bwalo lonse la akuru; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.

6. Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukuru kocokera kumwamba.

7. Ndipo ndinagwapansitu, ndipondinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilonda-londeranii Ine?

8. Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa Ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.

9. Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamva mau akulankhula nane.

10. Ndipo ndinati, ndidzacita ciani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Taukavpita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzicite.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 22