Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 22:11-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo popeza sindinapenya, cifukwa ca ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

12. Ndipo munthu dzina lace Hananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa cilamulo, amene amcitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,

13. anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.

14. Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe cifuniro cace, nuone Wolungamayo, numve mau oturuka m'kamwa mwace.

15. Ndipo udzamkhalira iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.

16. Ndipo tsopano ucedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kucotsa macimo ako, nuitane pa dzina lace.

17. Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera m'Kacisi, ndinacita ngati kukomoka,

18. ndipo ndinamuona iye, nanena nane, Fulumira, turuka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.

19. Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu;

20. ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kubvomerezana nao, ndi kusunga Zoobvala za iwo amene anamupha iye.

21. Ndipo anati kwa ine, Pita; cifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.

22. Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Acoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

23. Ndipo pakupfuula iwo, ndi kutaya zobvala zao, ndi kuwaza pfumbi mumlengalenga,

24. kapitao wamkuru analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe cifukwa cace nciani kuti ampfuulira comweco.

25. Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodinkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wace wosamveka?

26. Ndipo pakumva ici kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkuru, namuuza, nanena, Nciani ici uti ucite? pakuti munthuyo ndiye Mroma.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 22