Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 21:33-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?

34. Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

35. Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikari cifukwa ca kulimbalimba kwa khamulo;

36. pakuti unyinji wa anthu unatsata, nupfuula, Mcotse iye.

37. Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkuru, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Cihelene?

38. Si ndiwe M-aigupto uja kodi, unacita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kucipululu?

39. Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Kilikiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.

40. Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala cete onse, analankhula nao m'cinenedwe ca Cihebri, nanena.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 21