Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 21:32-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo posacedwa iye anatenga asilikari ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkuru ndi asilikari, analeka kumpanda Paulo.

33. Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?

34. Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

35. Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikari cifukwa ca kulimbalimba kwa khamulo;

36. pakuti unyinji wa anthu unatsata, nupfuula, Mcotse iye.

37. Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkuru, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Cihelene?

38. Si ndiwe M-aigupto uja kodi, unacita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kucipululu?

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 21