Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 20:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Trowa.

6. Ndipo tinapita m'ngalawa kucokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda cotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Trowa; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.

7. Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.

8. Ndipo munali nyali zambiri m'cipinda ca pamwamba m'mene tinasonkhanamo.

9. Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.

10. Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musacite phokoso, pakuti moyo wace ulipo.

11. Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kuca, anacokapo,

12. Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukuru.

13. Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira comweco, koma anati ayenda pamtunda yekha.

14. Ndipo pamene anakomana ndi ife ku Aso, tinamlandira, ndipo tinafika ku Mitilene.

15. Ndipo m'mene tidacokerapo, m'mawa mwace tinafika pandunjipa Kiyo; ndi m'mawa mwace tinangokoceza ku Samo, ndi m'mawa mwace tinafika ku Mileto.

16. Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.

17. Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.

18. Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo,Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 20