Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 20:35-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. M'zinthu zonse ndinakupatsani citsanzo, cakuti pogwiritsa nchito, koteromuyenerakuthandiza ofoka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

36. Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.

37. Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pace, nampsompsona,

38. nalira makamaka cifukwa ca mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yace. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 20