Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 2:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ocokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo.

6. Koma pocitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'cilankhulidwe cace ca iye yekha.

7. Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?

8. ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'cilankhulidwe cathu cimene tinabadwa naco?

9. Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya;

10. m'Frugiya, ndiponso m'Pamfuliya, m'Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo ocokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka,

11. Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikuru za Mulungu.

12. Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzace, Kodi ici nciani?

13. koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero.

14. Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ace, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ici cizindikirike kwa inu, ndi po cherani khutu mau anga.

15. Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lacitatulokha la tsiku;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 2