40. Ndipo ndi mau ena ambiri anacita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.
41. Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.
42. Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
43. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo 5 zozizwa ndi zizindikilo zambiri zinacitika ndi atumwi.
44. Ndipo onse akukhulupira anali pamodzi, 6 nakhala nazo zonse zodyerana.
45. Ndipo zimene anali nazo, ndi cuma cao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
46. Ndipo tsiku ndi tsiku 7 anali cikhalire ndi mtima umodzi m'Kacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;
47. nalemekeza Mulungu, 8 ndi kukhala naco cisomo ndi anthu onse. Ndipo 9 Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.