Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 2:38-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

39. Pakuti lonjezano 1 liri kwa inu, ndi kwa ana anu, 2 ndi kwa onse akutali, 3 onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

40. Ndipo ndi mau ena ambiri anacita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.

41. Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

42. Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

43. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo 5 zozizwa ndi zizindikilo zambiri zinacitika ndi atumwi.

44. Ndipo onse akukhulupira anali pamodzi, 6 nakhala nazo zonse zodyerana.

45. Ndipo zimene anali nazo, ndi cuma cao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.

46. Ndipo tsiku ndi tsiku 7 anali cikhalire ndi mtima umodzi m'Kacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;

47. nalemekeza Mulungu, 8 ndi kukhala naco cisomo ndi anthu onse. Ndipo 9 Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 2