Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 2:30-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi Iumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa cipatso ca m'cuuno mwace adzakhazika wina pa mpando wacifumu wace;

31. iye pakuona ici kale, analankhula za kuuka kwa Kristu, kuti sanasiyidwa m'Hade, ndipo thupi lace silinaona cibvunde.

32. Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ici tiri mboni ife tonse.

33. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja Lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ici, cimene inu mupenya nimumva.

34. Pakuti Davine sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha,Ambuye anati kwa Mbuye wanga,Khalani ku dzanja lamanja langa,

35. Kufikira ndikaike adani ako copondapo mapazi ako.

36. Pamenepo lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampacika.

37. Koma pamene anamva ici, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzacita ciani, amuna inu, abale?

38. Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

39. Pakuti lonjezano 1 liri kwa inu, ndi kwa ana anu, 2 ndi kwa onse akutali, 3 onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

40. Ndipo ndi mau ena ambiri anacita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.

41. Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

42. Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

43. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo 5 zozizwa ndi zizindikilo zambiri zinacitika ndi atumwi.

44. Ndipo onse akukhulupira anali pamodzi, 6 nakhala nazo zonse zodyerana.

45. Ndipo zimene anali nazo, ndi cuma cao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.

46. Ndipo tsiku ndi tsiku 7 anali cikhalire ndi mtima umodzi m'Kacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 2