Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 19:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?

16. Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amarisece ndi olasidwa.

17. Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Yesu Iinakuzika.

18. Ndipo ambiri a iwo akukhulipirawo anadza, nabvomereza, nafotokoza macitidwe ao.

19. Ndipo ambiri a iwo akucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wace, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

20. Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika.

21. Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wace, atapita pa Makedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.

22. Pamene anatuma ku Makedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi m'Asiya.

23. Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.

24. Pakuti munthu wina dzina lace Demetriyo wosula siliva, amene anapanga tiakacisi tasiliva ta Artemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri;

25. amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a nchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza cuma cathu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 19