Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 16:33-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.

34. Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.

35. Kutaca, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.

36. Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu turukani, mukani mumtendere.

37. Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ire pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ire amene tiri Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutiturutsira ire m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atiturutse.

38. Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.

39. Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawaturutsa, anawapempha kuti acoke pamudzi.

40. Ndipo anaturukam'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidiya: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 16