Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 15:28-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Pakuti cinakomer a Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu cothodwetsa cacikuru cina coposa izi zoyenerazi;

29. kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

30. Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.

31. Pamene anawerenga, anakondwera cifukwa ca cisangalatso cace.

32. Ndipo Yuda ndi Sila, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.

33. Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza. [

34. ]

35. Koma Paulo ndi Bamaba anakhalabe m'Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.

36. Patapita masiku, Paulo anati kwa Bamaba, Tibwerenso, tizonde abale m'midzi yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.

37. Ndipo Bamaba anafuna kumtenga Yohane uja, wochedwa Marko.

38. Koma sikunamkomera Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nao kunchito.

39. Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzace; ndipo Bamaba anatenga Marko, nalowa n'ngalawa, nanka ku Kupro.

40. Koma Paulo anasankha Sila, namuka, woikizidwa ndi abale ku cisomo ca Ambuye.

41. Ndipo iye anapita kupyola pa Suriya ndi Kilikiya, nakhazikitsa Mipingo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 15