Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 15:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Atumwi ndi abale akuru kwa abale a mwa amitundu a m'Antiokeya, ndi Suriya, ndi Kilikiya, tikulankhulani:

24. Popeza tamva kuti ena amene anaturuka mwa ife anakubvutani ndi mau, nasoceretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;

25. cinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Bamaba ndi Paulo,

26. anthu amene anapereka moyo wao cifukwa ca dzina la Yesu Kristu Ambuye wathu.

27. Tatumiza tsono Yuda ndi Sila, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.

28. Pakuti cinakomer a Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu cothodwetsa cacikuru cina coposa izi zoyenerazi;

29. kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

30. Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 15