Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 14:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakunena izo, anabvutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.

19. Ndipo anafika kumeneko Ayuda kucokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulomiyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.

20. Koma pamene, anamzinga akuphunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwace anaturuka ndi Bamaba kunka, ku Derbe.

21. Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri akuphunzira, anabwera ku Lustra ndi Ikoniyo ndi Antiokeya,

22. nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandauliraiwo kuti akhalebe m'cikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

23. Ndipo pamene anawaikira akuru mosankha mu Mpingo Mpingo, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, anaikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.

24. Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfuliya.

25. Ndipo atalankhula mau m'Perge, anatsikira ku Ataliya;

26. komweko anacoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku cisomo ca Mulungu ku Ilchito imene adaimarizayo,

27. Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anacita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la cikhulupiriro.

28. Ndipo anakhala pamenepo ndi akuphunzira nthawi yaikuru.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 14