28. Ndipo ngakhale sanapeza cifukwa ca kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.
29. Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda.
30. Koma Mulungu anamuukitsa iye kwa akufa;
31. ndipo 1 anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza iye pokwera ku Yerusalemu kucokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumcitira umboni tsopano kwa anthu.
32. Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa 2 lonjezano locitidwa kwa makolo;
33. kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salmo laciwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.
34. Ndipo kuti anamuukitsa iye kwa akufa, wosabweranso kueibvundi, anateropo, 3 Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davine.
35. Cifukwa anenanso m'Salmo lina, 4 Simudzapereka Woyera wanu aone cibvundi.
36. Pakutitu, Davine, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwace mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ace, naona cibvundi;
37. koma iye amene Mulungu anamuukitsa sanaona cibvundi.
38. Potero padziwike ndi inu amuna abale, 5 kuti mwa iye cilalikidwa kwa inu cikhululukiro ca macimo;
39. ndipo 6 mwa iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama kumcotsera zonse zimene simunangathe kudzicotsera poyesedwa wolungama ndi cilamulo ca Mose.
40. Cifukwa cace penyerani, kuti cingadzere inu conenedwa ndi anenenwo: