Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 12:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo m'mene anagogoda pa citseko ca pakhomo, linadza kudzabvomera buthu, dzina lace Roda.

14. Ndipo pozindikira mau ace a Petro, cifukwa ca kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.

15. Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wace.

16. Koma Petro anakhala cigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa.

17. Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale cete, anawafotokozera umo, adamturutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi, Ndipo anaturuka napita kwina.

18. Koma kutaca, panali phokoso lalikuru mwa asilikari, Petro wamuka kuti.

19. Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kaisareya, nakhalabe kumeneko.

20. Koma Herode anaipidwa nao a ku Turo ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zocokera ku dziko la mfumu.

21. Ndipo tsiku lopangira Herode anabvala zobvala zacifumu, nakhala pa mpando wacifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.

22. Ndipo anthu osonkhanidwawo anapfuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai.

23. Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, cifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.

24. Koma mau a Mulungu anakula, nacurukitsa.

25. Ndipo Bamaba ndi Saulo anabwera kucokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 12