Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 11:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo ici cinacitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.

11. Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ocokera ku Kaisareya.

12. Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;

13. ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yace, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;

14. amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse.

15. Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.

16. Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

17. Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Kristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 11