7. Ndipo m'mene atacoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ace awiri, ndi msilikari wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;
8. ndipo m'mene adawafotokozerazonse, anawatuma ku Yopa.
9. Koma m'mawa mwace, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lacisanu ndi cimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;
10. koma m'mene analikumkonzera cakudya kudamgwera ngati kukomoka;