Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. acerezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yace iri m'mbali mwa nyanja.

7. Ndipo m'mene atacoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ace awiri, ndi msilikari wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;

8. ndipo m'mene adawafotokozerazonse, anawatuma ku Yopa.

9. Koma m'mawa mwace, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lacisanu ndi cimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;

10. koma m'mene analikumkonzera cakudya kudamgwera ngati kukomoka;

11. ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi cotengera cirinkutsika, conga ngati cinsaru cacikuru, cogwiridwa pa ngondya zace zinai, ndi kutsikira padziko pansi;

12. m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga.

13. Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, nudye.

14. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10