Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:44-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Petro ali cilankhulire, 5 Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.

45. Ndipo 6 anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, cifukwa pa 7 amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.

46. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,

47. Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera 8 ngatinso ife?

48. Ndipo analamulira iwo 9 abatizidwe m'dzina la Yesu Kristu, Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10