Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:34-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo Petro anatsegula pakamwa pace, nati:Zoona ndizinkidira kuti Mulungu alibe tsankhu;

35. koma m'mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakucita cilungamo alandiridwa naye.

36. Mau amene anatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Kristu (ndiye Ambuye wa onse)

37. mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira;

38. za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nacita zabwino, naciritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi iye.

39. Ndipo ife ndife mboni zazonse adazicita m'dzikola Ayuda ndim'Yerusalemu; amenenso anamupha, nampacika pamtengo,

40. Ameneyo, Mulungu anamuukitsa tsiku lacitatu, nalola kuti aonetsedwe,

41. si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, 1 ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.

42. Ndipo 2 anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo ticite umboni kuti 3 Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.

43. 4 Ameneyu aneneri onse amcitira umboni, kuti onse akumkhulupirira iye adzalandira cikhululukiro ca macimo ao, mwa dzina lace.

44. Petro ali cilankhulire, 5 Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.

45. Ndipo 6 anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, cifukwa pa 7 amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.

46. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10