Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:3-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lacisanu ndi cinai la usana, nanena naye, Komeliyo.

4. Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nciani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zacifundo zako zinakwera zikhala cikumbutso pamaso pa Mulungu.

5. Ndipo tsopano tumiza amuna ku Y opa, aitane munthu Simoni, wochedwanso Petro;

6. acerezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yace iri m'mbali mwa nyanja.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10