Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali munthu ku Kaisareya, dzina lace Komeliyo, kenturiyo wa gulu lochedwa la Italiya,

2. ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lace lonse, amene anapatsa anthu zacifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.

3. Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lacisanu ndi cinai la usana, nanena naye, Komeliyo.

4. Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nciani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zacifundo zako zinakwera zikhala cikumbutso pamaso pa Mulungu.

5. Ndipo tsopano tumiza amuna ku Y opa, aitane munthu Simoni, wochedwanso Petro;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10