Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 1:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?

7. Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha.

8. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.

9. Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao.

10. Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao;

11. amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

12. Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kucokera ku phiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 1