23. Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wochedwa Barsaba, amene anachedwanso Yusto, ndi Matiya.
24. Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikiramitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,
25. alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kucokera komwe Yudase anapatukira, kuti apite ku malo a iye yekha.
26. Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiya; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.