Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 1:17-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Cifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lace la utumiki uwu.

18. (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphoto ya cosalungama; ndipo anagwa camutu, naphulika pakati, ndi matumbo ace onse anakhuthuka;

19. ndipo cinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m'manenedwe ao kadzikoka kanachedwa Akeldama, ndiko, kadziko ka mwazi.)

20. Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo,Pogonera pace pakhale bwinja,Ndipo pasakhale munthu wogonapo;Ndipo uyang'aniro wace autenge wina.

21. Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife,

22. kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwace pamodzi ndi ife.

23. Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wochedwa Barsaba, amene anachedwanso Yusto, ndi Matiya.

24. Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikiramitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,

25. alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kucokera komwe Yudase anapatukira, kuti apite ku malo a iye yekha.

26. Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiya; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 1